Genesis 29:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbalewace wa atate wace, kuti ndiye mwana wace wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wace.