Genesis 29:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wace, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwace. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.