Genesis 29:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafikako adaona chitsime ku busa, ndiponso magulu atatu a nkhosa zitagona pambali pa chitsimecho. Nkhosazo zinkamwa m'chitsime chimenechi chomwe pamwamba pake panali mwala waukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika kumeneko anaona chitsime ku busa ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pafupi ndi chitsimecho chifukwa nkhosazo zimamwetsedwa madzi ochokera mʼchitsimecho. Pamwamba pa chitsimecho panali mwala waukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayang'ana, taonani, citsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pacitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa citsime unali waukuru.