Genesis 29:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yakobo anati kwa Labani, “Nthawi yanga ndakwanitsa, ndipatseni mwana wanu kuti ndimukwatire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.