Genesis 29:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Zilipa kwa Leya.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Labani anapereka wantchito wake wamkazi Zilipa kwa Leya kuti akhale wantchito wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Leya.