Genesis 29:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.