Genesis 29:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Chauta wandipatsanso mwana wamwamunayu, chifukwa choti adamva kuti mwamuna wanga ine sandikonda.” Motero mwanayo adamutcha Simeoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakhalanso ndi pathupi ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Yehova anamva kuti mwamuna wanga sakundikonda, choncho wandipatsanso mwana winayu.” Ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Cifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamucha dzina lace Simeoni.