Genesis 29:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenganso pena pathupi, nabalanso mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano mwamuna wanga azindikonda kwambiri, popeza kuti ndamubalira ana aamuna atatu.” Motero mwanayo adamutcha Levi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine cifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; cifukwa cace anamucha dzina lace Levi.