Genesis 29:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenganso pathupi pena, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna, iye anati, “Nthawi ino ndidzalemekeza Yehova.” Choncho anamutcha Yuda. Kenaka analeka kubereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; cifukwa cace anamucha dzina lace Yuda; pamenepo analeka kubala.