Genesis 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo njoka inali yakucenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu, Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?