Genesis 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamarisece? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?