Genesis 3:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Ciani cimene wacitaci? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.