Genesis 3:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoŵeta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwaŵa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Cifukwa kuti wacita ici, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako: