Genesis 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti, “Ndidzaonjeza zovuta zako pamene udzakhala ndi pathupi, udzamva zoŵaŵa pa nthaŵi yako ya kubala mwana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mkaziyo Iye anati, “Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzacurukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.