Genesis 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa Adamu ndipo anati, Cifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa cifukwa ca iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: