Genesis 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atampirikitsira kunja Adamuyo, Mulungu adaika akerubi kuvuma kwa munda wa Edeni. Adaikanso lupanga lamoto limene linkazungulira mbali zonse, kutchinjiriza mtengo wopatsa moyo uja, kuti wina asaufike pafupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi ca kum'mawa kwace kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.