Genesis 3:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu amadziŵa kuti inu mukadzadya zipatso zimenezi, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala monga momwe aliri Mulunguyo. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.