Genesis 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zace, nadya, napatsanso mwamuna wace amene ali nave, nadya iyenso,