Genesis 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amarisece: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira mateweta.