Genesis 30:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo, ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni anapita ku munda ndipo anapezako zipatso za mankhwala wobereketsa. Tsono anatengerako mayi wake Leya. Rakele anati kwa Leya, “Chonde patseko mankhwala wakupezera mwana wakowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a cikondi m'thengo, nazitengera kwa amace Leva, Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.