Genesis 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.” Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpacabe kuti iwe wacotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kucotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Cifukwa cace iye adaagona nawe usiku uno cifukwa ca mankhwala a mwana wako.