Genesis 30:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho pamene Yakobo ankabwera kuchokera ku munda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nati, “Lero mukagona ku nyumba chifukwa ndakubwerekani ndi mankhwala wobereketsa a mwana wanga.” Choncho usiku umenewo Yakobo anakalowa kwa Leya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anadza madzulo kucokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine cifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.