Genesis 30:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adati, “Mulungu wandipatsa mphotho yokoma. Tsopano mwamuna wanga adzakhala nane chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Motero mwanayo adamutcha Zebuloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopane mwamuna wanga adzakhala ndi ine, cifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamucha dzina lace Zebuloni.