Genesis 30:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patseni akazi anga ndakugwirirani ntchitoŵa, pamodzi ndi ana anga, ndipo ndichoke. Mukudziŵa kuti ndakugwirirani bwino ntchito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patseni akazi anga ndi ana anga, amene ndinakugwirirani ntchito, ndipo ndidzanyamuka ulendo. Inu mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Undipatse ine akazi anga ndi ana anga cifukwa ca iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: cifukwa udziwa iwe nchito imene ndinakugwirira iwe.