Genesis 30:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patsogolo pake mudzazindikira ngati ndachita zimenezi mokhulupirika pamene mubwere kudzaona malipiro anga. Mukadzaona kuti ndili ndi mbuzi yopanda mathotho kapena maŵanga kapena mwanawankhosa amene sali wakuda, mudzadziŵe kuti imeneyo ndi yakuba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chilungamo changa chidzaoneka mʼtsogolo, pamene inu mudzabwere kudzaona malipiro angawo. Ngati mudzapeza mbuzi mʼgulu langa imene si yamawangamawanga, kapena mwana wankhosa wamkazi amene si wakuda ndiye kuti zimenezo zidzakhala kuti ndinakuberani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cotero cilungamo canga cidzandibvomereza m'tsogolomo, pamene udzandifika cifukwa ca malipiro amene ali patsogolo pako; iri yonse yosakhala yamathotho-mathotho ndi yamaanga-maanga ya mbuzi, ndi iri yonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.