Genesis 30:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsiku limenelo, Labani adachotsa atonde onse amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga, kudzanso mbuzi zazikazi zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga, zonse za maŵanga oyera. Adachotsanso nkhosa zonse zakuda, nauza ana ake kuti aziyang'anire zoŵeta zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake amuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde onse ndi mbuzi zazikazi zonse zimene zinali ndi mawangamawanga kapena zamathothomathotho, ndiponso zonse zabanga loyera. Anachotsa ana onse ankhosa aakazi akuda, napereka ziweto zonsezi kwa ana ake aamuna kuti aziweta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo Labani anacotsa atonde amene anali amipyololo-mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ace amuna.