Genesis 30:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthambizo adaziika patsogolo pa zoŵeta kumene zinkamwera madzi, kuti zoŵetazo ziziyang'ana nthambizo pomwa madzi, chifukwa zoŵetazo zinkakwerewa podzamwa madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatero anayika nthambi zija mʼmagome omwera madzi molunjika ziweto zija kuti pakumwa madziwo ziweto zazikazi ziziyangʼana nthambi zija popeza kuti pakumwa madzi ziweto zija zinkakwerana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'micera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo, ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.