Genesis 30:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adaika anaankhosa padera, naika nkhosa zina kuti ziyang'anane ndi zoŵeta za Labani zamathothomathotho ndi zakuda. Mwa njira imeneyi adapeza zoŵeta zakezake, ndipo sadazisokoneze ndi zoŵeta za Labani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anayika padera ana a ziweto zija. Koma ziweto zina anaziyika kuti ziyangʼanane ndi za Labani, zimene zinali za mawangamawanga ndi zakuda. Motero anapeza ziweto zakezake, ndipo sanazisakanize ndi za Labani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo analekanitsa ana a nkhosa naziika nkhope za zoweta kuti ziyang'anire zamipyololo-mipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani, ndipo anaika magulu ace pa okha; sanaziika pa zoweta za Labani.