Genesis 31:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adamva kuti ana a Labani ankanena kuti, “Yakobe watenga zonse za bambo wathu. Wapeza chuma chake m'chuma cha bambo wathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani ankanena kuti, “Yakobo watenga chilichonse cha abambo athu ndipo wapeza chuma chonsechi pogwiritsa ntchito chuma cha abambo athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yakobo afuna kwao nathawa nazo zace, Ndipo anamva mau a ana ace a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye cuma ici conse.