Genesis 31:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adati, ‘Tayang'ana, ndipo upenye kuti atonde onse amene akukweraŵa ndi amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Zimenezi ndachita ndine, popeza kuti ndaona zimene Labani akukuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anati, ‘Tayangʼana ndipo taona kuti atonde onse okwerana ndi ziweto ali amichocholozi, amawangamawanga kapena a mathothomathotho, popeza ndaona zonse zimene Labani wakhala akukuchitira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaangamaanga: cifukwa ndaona zonse zimene Labani akucitira iwe.