Genesis 31:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndine Mulungu amene ndidakuwonekera ku Betele kuja kumene udaimika mwala wachikumbutso ndi kuudzoza mafuta, ndipo kumeneko iwe udalumbira. Konzeka tsopano, uchoke kuno, ubwerere ku dziko lakwanu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndine Mulungu amene ndinadza kwa iwe pa Beteli paja. Beteli ndi kumalo kuja kumene unayimika mwala ndi kuwudzoza mafuta, komanso kulumbira kwa Ine. Tsopano choka mʼdziko lino msanga ndi kubwerera ku dziko la kwanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndine Mulungu wa ku Beteli, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine cilumbiriro: tsopano uka, nucoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.