Genesis 31:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zoŵeta zonse adazitsogoza namazikusa, pamodzi ndi zonse zimene adazipeza ku Mesopotamiya kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona m'Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anakusa ziweto zake zonse patsogolo natenga katundu wake yense amene anamupeza ku Padanaramu, ndipo ananyamuka kupita ku Kanaani, ku dziko la abambo ake, Isake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ananka nazo zoweta zace zonse, ndi cuma cace conse anacisonkhanitsa, zoweta zace anaziona m'Padan-aramu, kuti anke kwa Isake atate wace ku dziko la Kanani.