Genesis 31:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Labani adafunsa Yakobe kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kutenga ana anga aakazi ngati ogwidwa pa nkhondo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Labani anati kwa Yakobo, “Kodi ndakuchita chiyani kuti iwe undinamize ndi kutenga ana anga ngati anthu ogwidwa ku nkhondo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wacitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga.