Genesis 31:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili nazo mphamvu zakukuchita choipa. Koma usiku wapitawu, Mulungu wa atate ako wandiwuza kuti, ‘Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, ‘Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'dzanja langa muli mphamvu yakucitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.