Genesis 31:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mukapeza kuti wina aliyense pano ali ndi timilungu tanu, aphedwe ameneyo. Anthu tili nawoŵa akhale mboni pano pamene inu muyang'ane zinthu zanu m'katundu yenseyu. Tsono mukazipeza zanuzo mutenge.” Monsemo nkuti Yakobe ali wosadziŵa kuti Rakele adaaba timilunguto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mukapeza wina aliyense ndi milungu yanu, ameneyo sakhala ndi moyo. Anthu onse akupenya, lozani chilichonse chanu chimene chili ndi ine, ndipo ngati muchipeze tengani. Koma Yakobo sankadziwa kuti Rakele anabadi milunguyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ali yense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi movo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako ziri ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.