Genesis 31:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Labani adakaloŵa m'hema la Yakobe ndi m'hema la Leya ndiponso m'hema la adzakazi aŵiri aja, koma sadatipeze timilungu taketo. Kenaka adakaloŵa m'hema la Rakele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Labani analowadi mu tenti ya Yakobo, ya Leya ndi mʼmatenti a adzakazi awiri aja, koma sanapeze kalikonse. Atatuluka mu tenti ya Leya, analowa ya Rakele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze, Ndipo anaturuka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.