Genesis 31:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Rakeleyo anali ataibisa milungu ya m'nyumba mwa Labaniyo, ataiika pa chishalo cha pamsana pa ngamira, iyeyo nkukhala pomwepo. Labani adafunafuna m'hema monsemo, koma osaipeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamira, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Rakele anatengadi milungu ija ndi kuyiika mʼkati mwa chokhalira cha pa ngamira, iye nʼkukhalapo. Choncho Labani anafunafuna mu tenti monse koma wosapeza kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa cokhalira ca ngamila, nakhala pamenepo, Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze.