Genesis 31:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Rakele adauza bambo wake kuti, “Ngati ndikulephera kuimirira pamaso panu, musandikwiyire bambo, chifukwa sindili bwino malinga nza ife akazife.” Motero Labani adalephera kutipeza timilungu ta m'nyumba mwake tija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi zili pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rakele anati kwa abambo ake, “Pepanitu musandikwiyire mbuye wanga chifukwa choti sinditha kuyimirira pamaso panu chifukwa ndili kumwezi.” Choncho Labani anafunafuna koma sanayipeze milungu ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rakele anati kwa atate wace, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; cifukwa zocitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.