Genesis 31:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yakobe adapsa mtima kwambiri ndipo adalankhula ndi Labani mokalipa, adati, “Kodi ndakulakwirani chiyani? Kodi ndaphwanya lamulo lotani, kuti mundilondole?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anapsa mtima nafunsa Labani mwaukali kuti, “Kodi ndalakwa chiyani? Ndi tchimo lanji limene ndachita kuti muchite kundisaka chonchi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndacimwa ciani? ucimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?