Genesis 31:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwafunafuna m'katundu wanga yense, kodi mwapeza chiyani chanu? Chomwe mwapezacho muchiike poyera pano, kuti anthu anu ndi anthu angaŵa achiwone. Ndipo iwowo ndiwo aone wokhoza pakati pa aŵirife.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani mwafunyulula katundu wanga? Ndipo mwapeza chiyani cha inu pamenepa? Chimene mwapezapo chiyikeni poyera pamaso pa abale anu ndi anga kuti atiweruze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza ciani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika naco apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.