Genesis 31:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndi m'mene zidaaliri zinthu pa zaka makumi aŵiri zomwe ndidakhala ndi inu. Ndidakugwirirani ntchito zaka khumi ndi zinai chifukwa cha ana anu aŵiriŵa, ndipo zaka zisanu ndi chimodzi ndidagwirira zoŵeta. Komabe malipiro anga mwakhala mukusintha kakhumi konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zinthu zinali chonchi kwa zaka makumi awiri zimene ndinali mʼnyumba mwanu. Ndinakugwirirani ntchito kwa zaka khumi ndi zinayi chifukwa cha ana anu aakazi awiri ndipo zaka zina zisanu ndi chimodzi chifukwa cha ziweto zanu, ndipo munandisinthira malipiro kakhumi konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinakhala cotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe cifukwa ca ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi cimodzi cifukwa ca zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.