Genesis 31:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu wa atate anga, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu amene Isaki ankamuwopa, akadapanda kukhala nane, bwenzi mutandichotsa kale ndili chimanjamanja. Koma Mulungu adaona mavuto anga ndi ntchito za manja anga, ndipo usiku wapitawu Iye wakutsutsani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akanapanda kukhala nane Mulungu wa abambo anga, Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu amene Isake ankamuopa, mosakayika inu mukanandichotsa chimanjamanja. Koma Mulungu waona zovuta zanga ndi kulimbikira ntchito kwanga, ndipo usiku wapitawu anakudzudzulani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isake zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandicotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi nchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.