Genesis 31:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Labani adayankha Yakobe kuti, “Ana aakaziŵa ndi anga, ana ao ndi anga, pamodzi ndi zoŵeta zomwezi. Zonse ukuziwonazi nzanga. Koma tsopano ndiŵachitire chiyani ana anga aakaziŵa pamodzi ndi ana aoŵa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Labani anayankha Yakobo nati, “Ana aakaziwa ndi anga, ana awo ndi anganso. Ziwetozi ndi zanga. Chilichonse ukuona apa ndi changa. Koma tsopano ndingachite chiyani ndi ana anga aakaziwa kapena ndi ana awo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzacitira ine ciani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?