Genesis 31:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Labani adati, “Mulu wamiyalawu udzakhala chikumbutso kwa ine ndi iwe.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Galedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Labani anati, “Mulu uwu ndi mboni pakati pa inu ndi ine lero.” Ndi chifukwa chake unatchedwa Galeeda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Cifukwa cace anacha dzina lace, Galeeda;