Genesis 31:54 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anapereka nsembe pa phiri paja, ndipo anayitana abale ake kuti adzadye chakudya. Atadya chakudya anagona pa phiri pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ace kuti adye cakudya; ndipo anadya cakudya, nagona paphiripo usiku wonse.