Genesis 32:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine siwoyenera kulandira kukoma mtima kwanu ndi kukhulupirika kwanu kumene mwaonetsa wantchito wanu. Ndinali ndi ndodo yokha pamene ndinawoloka Yorodani uyu koma tsopano ndili ndi magulu awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamcitira kapolo wanu: cifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndiri makamu awiri.