Genesis 32:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkuru wanga, m'dzanja la Esau; cifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.