Genesis 32:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani lonjezo lanu lija lakuti, ‘Ndithu ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zosaŵerengeka. Zidzakhala zochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mchenga wa pa nyanja, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paja Inu munandilonjeza kuti simudzalephera kundichitira zabwino ndi kuti zidzukulu zanga zidzakhala zosawerengeka ngati mchenga wa ku nyanja.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Inu munati. Ndidzakucitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mcenga wa pa nyanja yaikuru, umene sungathe kuwerengeka cifukwa ca unyinji wace.