Genesis 32:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkuru wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? za yani zimenezi patsogolo pako?