Genesis 32:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.